1 Chronicles 29:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo atsogoleri a mabanja a makolo adapereka zopereka zao mwaufulu, monga momwe adachitiranso atsogoleri a mafuko, atsogoleri a magulu a anthu zikwi, atsogoleri a magulu a anthu mazana ndiponso akapitao a ntchito za mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo akulu a nyumba za makolo, ndi akulu a mafuko a Israele, ndi akulu a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira ntchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo akuru a nyumba za makolo, ndi akuru a mafuko a Israyeli, ndi akuru a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira nchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,