1 Chronicles 3:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana asanu ndi mmodzi onseŵa adabadwira ku Hebroni, kumene adakhala mfumu pa zaka zisanu ndi ziŵiri ndi miyezi isanu ndi umodzi. Koma adakhala mfumu ku Yerusalemu zaka 33.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anambadwira asanu ndi mmodzi m'Hebroni; ndi pomwepo anakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri, ndi miyezi isanu ndi iwiri; ndi m'Yerusalemu anakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zitatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi. Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anambadwira asanu ndi mmodzi m'Hebroni; ndi pomwepo anakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri, ndi miyezi isanu ndi iwiri; ndi m'Yerusalemu anakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zitatu.