1 Chronicles 4:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkazi wake Wachiyuda adamubalira Yeredi, bambo wa Gedori, Hebere bambo wa Soko, ndiponso Yekutiyele bambo wa Zanowa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mkazi wake Myuda anabala Yeredi atate wa Gedori, ndi Hebere atate wa Soko, ndi Yekutiyele atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mkazi wace Myuda anabala Yeredi atate wa Gedoro, ndi Heberi atate wa Soko, ndi Yekutiyeli atate wa Zanowa. Ndipo awa ndi ana a Bitiya mwana wamkazi wa Farao, amene Meredi anamtenga.