1 Chronicles 4:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunalinso Yokimu, pamodzi ndi amuna a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi amene ankalamula ku Mowabu, koma adabwerera ku Lehemu (tsono nkhani zimenezitu nzakalekale).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yowasi, ndi Sarafi wolamulira m'Mowabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale).
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi Yokimu, ndi amuna a Kozeba, ndi Yoasi, ndi Sarafa wolamulira m'Moabu, ndi Yasubilehemu; koma mau awa ndiwo a kale lomwe.