1 Chronicles 4:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Simei anali nawo ana aamuna 16, ndi ana aakazi asanu ndi mmodzi. Koma abale ake analibe ana ambiri, ndipo mabanja ao sadakule kufanana ndi anthu a ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ake analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinachulukitsa ngati ana a Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Simei anali nao ana amuna khumi mphambu asanu ndi mmodzi, ndi ana akazi asanu ndi mmodzi; koma abale ace analibe ana ambiri, ndi banja lao lonse silinacurukitsa ngati ana a Yuda.