1 Chronicles 4:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali munthu wina dzina lake Yabezi amene anthu ankamlemekeza kupambana abale ake. Mai wake pomutcha dzina la Yabezi ankanena kuti, “Chifukwa ndidamubala movutikira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ake; ndi make anamutcha dzina lake Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, “Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yabezi analemekezedwa koposa abale ace; ndi mace anamucha dzina lace Yabezi, ndi kuti, Popeza ndambala mwaululu.