1 Chronicles 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa ana a Rubeni, mwana wachisamba wa Israele. Inde Rubeni analidi mwana wachisamba, koma chifukwa adaagona ndi mkazi wina wamng'ono wa bambo wake, uchisamba wakewo udapatsidwa kwa Yosefe, mng'ono wake. Motero Rubeniyo saoneka pa mndandanda wa maina potsata za kubadwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israele, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wake ukulu wake unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israele, koma m'buku la chibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Rubeni mwana woyamba wa Israyeli, (pakuti ndiye mwana woyamba; koma popeza anaipsa kama wa atate wace ukulu wace unapatsidwa kwa ana a Yosefe mwana wa Israyeli, koma m'buku la cibadwidwe asayesedwe monga mwa ukulu wace.