1 Chronicles 5:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onseŵa adalembedwa potsata mibadwo yao pa nthaŵi ya Yotamu mfumu ya ku Yuda, ndiponso pa nthaŵi ya Yerobowamu mfumu ya ku Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a chibadwidwe chao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m'masiku a Yerobowamu mfumu ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onsewo anawerengedwa monga mwa mabuku a cibadwidwe cao, masiku a Yotamu mfumu ya Yuda, ndi m'masiku a Yerobiamu mfumu ya Israyeli.