1 Chronicles 5:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Arubeni, Agadi ndiponso theka la fuko la Manase anali ndi anthu olimba mtima odziŵa kumenya nkhondo ndi zishango, malupanga ndi mauta. Onse pamodzi anali 44,760, okonzekeratu kukamenya nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi limodzi la magawo awiri a fuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira chikopa ndi lupanga, ndi kuponya mivi, ozolowera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akutuluka kunkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a Rubeni, ndi a Gadi, ndi limodzi la magawo awiri a pfuko la Manase, ngwazi, amuna akugwira cikopa ndi lupanga, ndi kuponya mibvi, ozerewera nkhondo, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zinai mphambu mazana asanu ndi awiri kudza makumi asanu ndi limodzi akuturuka kunkhondo.