1 Chronicles 5:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu adaŵathandiza pomenya nkhondoyo, ndipo Ahagiriwo pamodzi ndi onse amene adaaphatikana nawo, adaperekedwa m'manja mwao. Ankalira kwa Mulungu pomenya nkhondoyo, tsono Mulungu adaŵapatsa zimene ankapemphazo, popeza kuti adaamkhulupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagiri anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anafuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anathandizidwa polimbana nao; ndi Ahagari anaperekedwa m'dzanja lao, ndi onse anali nao; pakuti anapfuulira kwa Mulungu pomenyana nao, ndipo anapembedzeka nao, popeza anamkhulupirira iye.