1 Chronicles 5:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu aja adachimwira Mulungu wa makolo ao, nadzipereka kwa milungu ya anthu am'dzikomo amene Mulungu adaŵaononga iwowo akufika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma analakwira Mulungu wa makolo ao, nachita chigololo, ndi kutsata milungu ya mitundu ya anthu a m'dziko, amene Mulungu adaononga pamaso pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma analakwira Mulungu wa makolo ao, nacita cigololo, ndi kutsata milungu ya mitundu ya anthu a m'dziko, amene Mulungu adaononga pamaso pao.