1 Chronicles 5:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mulungu wa Israele adautsa mtima wa Pulo mfumu ya ku Asiriya, amene dzina lake lina linali Tigilati-Pilesere, ndipo adaŵatenga Arubeni, Agadi ndiponso theka la fuko la Manase, napita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi fuko la Manase logawika pakati, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mulungu wa Israyeli anautsa mzimu wa Puli mfumu ya Asuri, ndi mzimu wa Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.