1 Chronicles 6:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankatumikira akuimba nyimbo pakhomo pa malo opatulika a m'chihema chamsonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu. Ndipo ankagwira ntchito yao yotumikirayo potsata malamulo amene adaaŵapatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatumikira ndi kuimba pakhomo pa Kachisi wa chihema chokomanako mpaka Solomoni adamanga nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, naimirira m'utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anatumikira ndi kuyimba pakhomo pa kacisi wa cihema cokomanako mpaka Solomo adamanga nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, naimirira m'utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.