1 Chronicles 6:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ameneŵa ndiwo anthu amene ankatumikira pamodzi ndi ana ao aamuna. Pa banja la Kohati panali Hemani, katswiri woimba. Mndandanda wa mibadwo yao unali motere: Hemani anali mwana wa Yowele, mwana wa Samuele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woimbayo, mwana wa Yowele, mwana wa Samuele,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa: Ochokera ku banja la Kohati: Hemani, katswiri woyimba, anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woyimbayo, mwana wa Yoeli, mwana wa Samueli,