1 Chronicles 6:49 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Aroni pamodzi ndi ana ake ankapereka nsembe pa guwa la nsembe zopsereza, ndi pa guwa lofukizirapo lubani. Iwowo ndiwo ankachita ntchito zonse zoyenera malo opatulika kwambiri, ndi kuchita mwambo wolipirira machimo a Aisraele. Ankachita zimenezi potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu adaŵalamula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Aroni ndi ana ake ankafukiza pa guwa la nsembe yopsereza, ndi pa guwa la nsembe yofukiza, chifukwa cha ntchito yonse ya malo opatulika kwambiri, ndi kuchitira Israele chowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Aroni ndi ana ace adafofukiza pa guwa la nsembe yopsereza, ndi pa guwa la nsembe yofukiza, cifukwa ca nchito yonse ya malo opatulikitsa, ndi kucitira Israyeli cowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.