1 Chronicles 7:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makiri adapezera Hupimu ndi Supimu akazi, wina wake wina wake. Mlongo wake anali Maaka. Dzina la wachiŵiriyo linali Zelofehadi. Ndipo Zelofehadiyo anali ndi ana aakazi okhaokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wake wa Hupimu ndi Supimu, dzina lake ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana wachiwiri wa Manase ndiye Zelofehadi. Ndi Zelofehadi anali ndi ana akazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka. Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi Makiri anadzitengera mkazi, mlongo wace wa Hupimu ndi Supimu, dzina lace ndiye Maaka. Ndipo dzina la mwana waciwiri wa Manase ndiye Tselofekadi. Ndi Tselofekadi anali ndi ana akazi.