1 Chronicles 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Tola naŵa: Uzi, Refaya, Yeriyele, Yamai, Ibisamu, ndi Semuele, atsogoleri a mabanja a makolo ao, ndiye kuti a banja la Tola. Onsewo anali ankhondo amphamvu pa mibadwo yao. Chiŵerengero chao pa nthaŵi ya Davide chinali 22,600.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Refaya, ndi Yeriyele, ndi Yamai, ndi Ibisamu, ndi Semuele, akulu a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao, masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a Tola ndi awa: Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Repaya, ndi Yerieli, ndi Yamai, ndi Ibsamu, ndi Semueli, akuru a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.