1 Chronicles 7:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Efuremu adakaloŵa kwa mkazi wake, ndipo mkaziyo adatenga pathupi nabala mwana. Mwanayo adamutcha dzina loti Beriya, chifukwa chakuti tsoka lidaagwera banja lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo analowa kwa mkazi wake, naima iye, nabala mwana, namutcha dzina lake Beriya, popeza m'nyumba mwake mudaipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anagona ndi mkazi wake, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Beriya, chifukwa tsoka linagwera banja lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo analowa kwa mkazi wace, naima iye, nabala mwana, namucha dzina lace Beriya, popeza m'nyumba mwace mudaipa.