1 Chronicles 7:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zidzukulu za Manase zinkalamulira mizinda iyi: Beteseani pamodzi ndi midzi yake, Tanaki pamodzi ndi midzi yake, Megido pamodzi ndi midzi yake, Dori pamodzi ndi midzi yake. Kumeneko ndiko kumene kunkakhala ana a Yosefe mwana wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi milaga yake, Taanaki ndi milaga yake, Megido ndi milaga yake, Dori ndi milaga yake. M'menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmbali mwa malire a Manase munali Beti-Seani, Taanaki, Megido ndi Dori, pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Yosefe mwana wa Israeli zimakhala mʼmizinda imeneyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi miraga yace, Taanaki ndi miraga yace, Megido ndi miraga yace, Dora ndi miraga yace. M'menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israyeli.