1 Chronicles 7:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onseŵa anali zidzukulu za Asere. Anali atsogoleri a mabanja a makolo ao, anthu omveka, ankhondo amphamvu, akuluakulu pakati pa akalonga. Chiŵerengero chao cholembedwa m'buku, potsata mibadwo yao yoyenera ntchito yankhondo, chinali 26,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Awa onse ndiwo ana a Asere, akulu a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akulu mwa akalonga. Oyesedwa mwa chibadwidwe chao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onsewa anali zidzukulu za Aseri, atsogoleri a mabanja, anthu omveka, ankhondo olimba mtima, ndi akuluakulu pakati pa atsogoleri anzawo. Chiwerengero cha anthu odziwa kumenya nkhondo chomwe chinalembedwa chinali 26,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Awa onse ndiwo ana a Aseri, akuru a nyumba za makolo ao, ngwazi zosankhika ndi zamphamvu, akuru mwa akalonga. Oyesedwa mwa cibadwidwe cao otumikira kunkhondo ndiwo amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi cimodzi.