1 Chronicles 7:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale ao a mabanja onse a Isakara analipo onse pamodzi 87,000, ankhondo amphamvu, olembedwa potsata mibadwo yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi abale ao mwa mabanja onse a Isakara, ngwazi zamphamvu, oyesedwa mwa chibadwidwe chao, onsewa ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu zisanu ndi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi abale ao mwa mabanja onse a Isakara, ngwazi zamphamvu, oyesedwa mwa cibadwidwe cao, onsewa ndiwo zikwi zisanu ndi zitatu mphambu zisanu ndi ziwiri.