1 Chronicles 8:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Ulamu anali ankhondo amphamvu, anthu amauta, ndipo anali ndi ana ndi adzikulu 150. Onseŵa anali Abenjamini.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mivi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana a Ulamu anali asilikali olimba mtima amene amadziwa kugwiritsa ntchito uta. Iwo anali ndi ana ndi adzukulu ambiri ndipo onse analipo 150. Onsewa anali adzukulu a Benjamini.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mibvi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.