1 Chronicles 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana a Ehudi amene anali atsogoleri a mabanja okhala ku Geba, adachotsedwa kwaoko ndipo adakakhala ku Manahati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akulu a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kunka ku Manahati,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zidzukulu za Ehudi, zimene zinali atsogoleri a mabanja a amene amakhala ku Geba ndipo zinasamutsidwa kupita ku Manahati zinali izi:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ana a Ehudi ndi awa: ndiwo akuru a nyumba za makolo ao a iwo okhala ku Geba, ndipo anawatenga ndende kumka ku Manahati,