1 Chronicles 9:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Aisraele onse adalembedwa potsata mibadwo yao m'buku la mafumu a Aisraele. Anthu a ku Yuda adaatengedwa ukapolo kunka ku Babiloni chifukwa chakuti anali osakhulupirika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli. Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Aisrayeli onse anawerengedwa mwa cibadwidwe cao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israyeli; ndipo Yuda anatengedwa ndende kumka ku Babulo cifukwa ca kulakwa kwao.