1 Chronicles 9:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja, ankayang'anira ntchito ya utumiki pakhomo pa chihema, monga ankachitira azibambo ao, amene ankayang'anira mudzi wazithando wa Chauta ndi kulonda pa chipata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, ndi abale ake a nyumba ya atate wake; Akora anayang'anira ntchito ya utumiki, osunga zipata za Kachisi monga makolo ao; anakhala m'chigono cha Yehova osunga polowera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiasafu; mwana wa Kora, ndi abale ace a nyumba ya atate wace; Akora anayang'anira nchito ya utumiki, osunga zipata za kacisi monga makolo ao; anakhala m'cigono ca Yehova osunga polowera;