1 Chronicles 9:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onseŵa, amene adasankhidwa kuti akhale alonda apamakomo, analipo 212. Adalembedwa potsata mibadwo yao ku midzi yao. Davide ndi Samuele mneneri ndiwo adaŵaika m'malo ao a ntchito chifukwa cha kukhulupirika kwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa chibadwidwe chao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samuele mlauli anawaika m'udindo wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene anasankhidwa kukhala alonda pa khonde analipo 212. Iwo analembedwa mwa mibado yawo ku midzi yawo. Davide ndi mneneri Samueli ndiwo anawayika mʼmalo awo antchito chifukwa cha kukhulupirika kwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo onse osankhidwa akhale odikira kuzipata ndiwo mazana awiri mphambu khumi ndi awiri. Iwo anawerengedwa monga mwa cibadwidwe cao, m'midzi mwao, amene Davide ndi Samueli mlauli anawaika m'udindo wao.