1 Chronicles 9:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pakuti atsogoleri anai a alonda apamakomo amene anali Alevi, ankayang'anira zipinda ndiponso mosungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti odikira anai akulu, ndiwo Alevi, anali m'udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo chuma m'nyumba ya Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma atsogoleri akuluakulu anayi a alonda, amene anali Alevi, anapatsidwa udindo woyangʼanira zipinda ndi chuma cha nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti odikira anai akuru, ndiwo Alevi, anali m'udindo wao, nayang'anira zipinda ndi mosungiramo cuma m'nyumba ya Mulungu.