1 Chronicles 9:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena mwa Aleviwo ankayang'anira ziŵiya za pa chipembedzo, pakuti kunali kofunika kuziŵerenga pozibweza kapena pozitulutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ena a iwo anayang'anira zipangizo za utumikiwo, pakuti analowa nazo ataziwerenga, natuluka nazo ataziwerenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena amayangʼanira zipangizo zimene amagwiritsa ntchito pa ntchito mʼNyumba ya Mulungu. Iwo amaziwerenga zikamalowetsedwa ndi potulutsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ena a iwo anayang'anira zipangizo za utumikiwo, pakuti analowa nazo ataziwerenga, naturuka nazo ataziwerenga.