1 Chronicles 9:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ena mwa iwowo adasankhidwa kuti aziyang'anira zipangizo ndi ziŵiya zina zopatulika. Ena ankayang'anira ufa wosalala, vinyo, mafuta, lubani ndiponso zonunkhira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ena a iwo anaikidwa ayang'anire zipangizo zilizonse, ndi zipangizo zonse za malo opatulika, ndi ufa wosalala, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi lubani, ndi zonunkhira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena anapatsidwa udindo wosamalira zipangizo ndi zinthu zina zonse za ku malo opatulika, pamodzi ndi ufa, vinyo, mafuta, lubani ndi zonunkhira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ena a iwo anaikidwa ayang'anire zipangizo ziti zonse, ndi zipangizo zonse za malo opatulika, ndi ufa wosalala, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi libano, ndi zonunkhira.