1 Chronicles 9:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi ena akuluakulu ankayang'anira oimba nyimbo. Iwowo ankakhala m'zipinda m'Nyumba ya Chauta, osamangika ndi ntchito zina, pakuti ankatumikira usana ndi usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo awa ndi oimba akulu a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku ntchito zina; pakuti anali nayo ntchito yao usana ndi usiku.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri a mabanja a Alevi, amene anali ndi luso loyimba, amakhala mʼzipinda za Nyumba ya Mulungu ndipo samagwira ntchito zina chifukwa ankatumikira usana ndi usiku.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo awa ndi oyimba akuru a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku nchito zina; pakuti anali nayo nchito yao usana ndi usiku.