1 Corinthians 1:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti chipusa cha Mulungu chiposa anthu ndi nzeru zao; ndipo chofooka cha Mulungu chiposa anthu ndi mphamvu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti copusa ca Mulungu ciposa anthu ndi nzeru zao; ndipo cofoka ca Mulunguciposa anthu ndi mphamvu yao.