1 Corinthians 10:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mkate ndiwo umodzi, chotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako kumkate umodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti buledi ndi mmodzi yekha, ifenso ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, popeza tonse timagawana buledi mmodzi yemweyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mkate ndiwo umodzi, cotero ife ambiri ndife thupi limodzi; pakuti ife tonse titengako ku mkate umodzi.