1 Corinthians 10:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkunja akakuitanani kuti mukadye naye, inuyo nkuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni. Musakafunse mafunso okhudzana ndi m'mene mtima wanu umamvera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati wina wa osakhulupirira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye chomwe chiikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, chifukwa cha chikumbu mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati wina wa osakhulupira akuitanani, ndipo mufuna kupita; mudye comwe ciikidwa kwa inu, osafunsa kanthu, cifukwa ca cikumbu mtima.