1 Corinthians 10:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma wina akakuuzani kuti, “Nyama iyi idaperekedwa kwa mafano,” apo ndiye musadye nyamayo. Chifukwa cha amene wakuuzayo, usadye nyamayo, kuwopa kuti mtima ungavutike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, chifukwa cha iyeyo wakuuza, ndi chifukwa cha chikumbu mtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati wina akati kwa inu, Yoperekedwa nsembe iyi, musadye, cifukwa ca iyeyo wakuuza, ndi cifukwa ca cikumbu mtima.