1 Corinthians 11:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zokuwonerani zimenezi! Kodi mulibe nyumba zomakadyeramo ndi kumweramo? Kodi kapena mufuna kunyazitsa Mpingo wa Mulungu ndi kuŵachititsa manyazi amene alibe kanthu, eti? Ndikuuzeni chiyani tsono? Ndingakuyamikeni ngati? Iyai, pa zimenezi sindingakuyamikeni konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Mpingo wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena chiyani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga mulibe nyumba za kudyeramo ndi kumweramo? Kapena kodi munyoza Eklesia wa Mulungu, ndi kunyoza iwo amene alibe kanthu? Ndidzanena ciani kwa inu? Kodi ndidzatama inu m'menemo? Sindikutamani.