1 Corinthians 11:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati wina ali ndi njala, ayambe wadya kwao, kuti Mulungu angakulangeni chifukwa cha kusonkhana kwanu. Koma zina zimene sindidatchule, ndidzazilongosola ndikabwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati wina ali ndi njala adye kwao; kuti mungasonkhanire kwa chiweruziro. Koma zotsalazo ndidzafotokoza pakudza ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo. Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati wina ali ndi njala adye-kwao; kuti mungasonkhanire kwa ciweruziro. Koma zotsalazo nelidzafotokoza pakudza ine.