1 Corinthians 11:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati mkazi sazivala kanthu kumutu, kunali bwino atangodula tsitsi lake. Koma popeza kuti nchamanyazi kwa mkazi kumeta mpala, kapena kudula tsitsi lake, ndiyetu azivala kanthu kumutu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati mkazi safunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kuchititsa manyazi, afunde.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati mkazi sapfunda, asengedwenso; koma ngati kusengedwa kapena kumetedwa kucititsa manyazi, apfunde,