1 Corinthians 11:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa mwamuna palibe chifukwa choti azivalira kanthu kumutu, pakuti amaonetsa maonekedwe ndi ulemerero wa Mulungu. Koma mkazi amaonetsa ulemerero wa mwamuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mwamuna sayenera kuvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mwamuna sayenera kubvala pamutu, popeza akhala fanizo ndi ulemerero wa Mulungu: koma mkazi ali ulemerero wa mwamuna.