1 Corinthians 12:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa wina mphamvu zochita zodabwitsa, kwa wina mawu a uneneri, kwa wina mphatso yozindikira mizimu, kwa wina malilime osiyanasiyana, ndiponso kwa wina kutanthauzira malilimewo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kwa wina macitidwe a mphamvu; ndi kwa wina cinenero; ndi kwa wina cizindikiro ca mizimu; kwa wina malilime a mitundu mitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.