1 Corinthians 12:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga phazi litanena kuti, “Poti sindine dzanja, ndiye kuti sindine chiwalo cha thupi”, kodi silikhala chiwalo cha thupi chifukwa cha chimenecho?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati phazi likati, Popeza sindili dzanja, sindili wa thupi; kodi silili la thupi chifukwa cha ichi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati phazi litanena kuti, “Pakuti sindine dzanja, sindine chiwalo cha thupi.” Chifukwa chimenechi sichingachititse phazi kuti lisakhale chiwalo cha thupi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati phazi likati, Popeza sindiri dzanja, sindiri wa thupi; kodi siliri la thupi cifukwa ca ici?