1 Corinthians 13:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndiribe cikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.