1 Corinthians 13:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati cimbuuzi; koma R pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa.