1 Corinthians 13:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndiri naco cikhulupiriro conse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndiribe cikondi, ndiri cabe.