1 Corinthians 14:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukayamika Mulungu ndi mtima wanu wokha, nanga munthu amene ali nanu pamodzi, koma sadziŵa zamumtimazo, angavomereze bwanji kuti, “Amen!” pa pemphero lanu lothokoza Mulungu, pamene sakudziŵa zimene inuyo mukunena.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa chimene unena?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mutamanda Mulungu mu mzimu, kodi munthu amene wapezeka pakati pa amene akuyankhula zomwe sakumva, adzavomereza bwanji kuti “Ameni” pa pemphero lanu loyamikalo popeza sakumva chimene mukunena?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ngati udalitsa ndi mzimu, nanga iye wakukhala wosaphunzira adzati Amen bwanji, pa kuyamika kwako, popeza sadziwa cimene unena?