1 Corinthians 14:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthutu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, salankhula ndi anthu ai, koma ndi Mulungu. Palibe munthu womvetsa zimene iyeyo akunena, Mzimu Woyera ndiye amamlankhulitsa zachinsinsi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti aliyense amene amayankhula malilime sayankhula kwa anthu, koma kwa Mulungu. Zoonadi, palibe amene amamva zimene akunena chifukwa Mzimu ndiye amamuyankhulitsa zachinsinsi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibemunthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.