1 Corinthians 14:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'Malembo mudalembedwa kuti, “Ndidzalankhula ndi mtundu uwu kudzera mwa anthu a zilankhulo zachilendo, ndiponso ndi pakamwa pa anthu achilendo. Koma ngakhale nditero, sadzandimvera, akutero Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zinalembedwa mʼMalamulo kuti, “Ndidzayankhula kwa anthu awa, kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo ndiponso ndi milomo yachilendo. Koma ngakhale nthawi imeneyo sadzandimvera Ine, akutero Ambuye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwalembedwa m'cilamulo, Ndi anthu amalilime ena ndipo ndi milomo yina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.