1 Corinthians 14:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngati mpingo wonse usonkhana pamodzi, ndipo onse ayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, nanga mukaloŵa anthu osadziŵa kapena osakhulupirira, kodi iwo sadzayesa kuti ndinu amisala?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupirira, kodi sadzanena kuti mwayaluka?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero kuti ngati mpingo wonse utasonkhana pamodzi ndipo aliyense namayankhula malilime, ndipo wina amene sangazindikire kapena ena osakhulupirira nabwerapo, kodi sadzanena kuti mwachita misala?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, ngati Mpingo wonse akasonkhane pamodzi, ndi onse akalankhule malilime, ndipo akalowemo anthu osaphunzira kapena osakhulupira, kodi sadzanena kuti mwayaruka?