1 Corinthians 14:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati palibe wotanthauzira, woyankhulayo akhale chete mu mpingo ndipo adziyankhulire iye mwini ndi Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati palibe womasulira, akhale cete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.