1 Corinthians 14:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati wina akuyesa kuti akulankhula mau ochokera kwa Mulungu, kapena kuti akuuzidwa mau ndi Mzimu Woyera, avomereze kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo lochokera kwa Ambuye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati wina ayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu, azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu zili lamulo la Ambuye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati wina aliyense akuganiza kuti ndi mneneri kapena kuti ali ndi mphatso za Mzimu, ayenera kudziwa kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo la Ambuye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngatiwinaayesa kuti ali mneneri, kapena wauzimu; azindikire kuti zimene ndilemba kwa inu ziri lamulo la Ambuye,