1 Corinthians 14:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale, mudzapindulanji ngati ndibwera kwa inu nkumadzalankhula m'zilankhulo zosadziŵika? Simudzapindula konse ndi kulankhula kwangako, ngati m'mau angawo mulibe zina zimene Mulungu wandiwululira, kapena zina zopatsa nzeru, kapena zina zimene Mulungu andipatsa kuti ndinene, kapenanso phunziro lina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikakupindulitsani chiyani, ngati sindilankhula ndi inu kapena m'vumbulutso, kapena m'chidziwitso, kapena m'chinenero, kapena m'chiphunzitso?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono, abale, mudzapindula chiyani nditabwera kwa inu ndi kukuyankhulani mʼmalilime? Koma mudzapindula ngati nditakubweretserani vumbulutso lina lake, kapena chidziwitso, kapena chiphunzitso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma tsopano, abale, ngati ndidza kwa inu ndi kulankhula malilime, ndikaku, pindulitsani ciani, ngati sindilankhui landi inu kapena m'bvumbulutso, kapena m'cidziwitso, kapena m'cinenero, kapena m'ciphunzitsot